Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 7:31 - Buku Lopatulika

31 Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Koma anthu ambiri a m'khamu limenelo adamkhulupirira, ndipo ankati, “Kodi akadzabwera Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzachita zizindikiro zozizwitsa zoposa zimene munthuyu wachita?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:31
19 Mawu Ofanana  

Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.


pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.


Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo?


Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.


Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.


Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa