Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake.
Tito 3:3 - Buku Lopatulika Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu kale ifenso tinali opusa, osamvera, ndi osokezedwa. Tinali akapolo a zilakolako zoipa ndi zisangalatso zamitundumitundu. Masiku onse tinkakhalira kuchita zoipa ndi kaduka, anthu kudana nafe, ndipo ife tomwe kumadana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. |
Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake.
Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.
Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?
Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?
Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.
Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.
Pakuti monga inunso kale simunamvere Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake:
Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho;
Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.
podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.
ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.
Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.