Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Obadiya 1:3 - Buku Lopatulika

3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali, iwe amene umanena mu mtima mwako kuti, ‘Ndani anganditsitse pansi?’

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:3
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.


Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.


Nalimbika mtima Amaziya. Natsogolera anthu ake, namuka ku Chigwa cha Mchere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.


Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.


Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo, nugunda pamitambo mutu wake;


Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.


Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.


Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?


Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka.


Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?


Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa paphiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa