Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Obadiya 1:4 - Buku Lopatulika

4 Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:4
8 Mawu Ofanana  

dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.


Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.


Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la choipa!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa