Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Obadiya 1:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:4
8 Mawu Ofanana  

Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”


Kuopseza kwako kwakunyenga; kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri. Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.


Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga ndi kulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,” akutero Yehova.


Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko. Ngakhale atakwera kumwamba Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.


“Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo, kukweza malo ake okhalapo, kuthawa mavuto!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa