Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Numeri 20:1 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mwezi woyamba, mpingo wonse wa Aisraele udafika ku chipululu cha Zini, ndipo anthuwo adakhala ku Kadesi. Miriyamu adafera kumeneko naikidwa komweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mwezi woyamba gulu lonse la Aisraeli linafika ku chipululu cha Zini, ndipo anakhala ku Kadesi. Miriamu anafera kumeneko ndipo anayikidwa mʼmanda. |
Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?
Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.
Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.
Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.
Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.
Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu.
Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.
Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori.
Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.
Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.
popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m'chipululu cha Zini.
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatule Ine pakati pa ana a Israele.
pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m'chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;