Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 13:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Choncho adapita kukazonda dzikolo kuyambira ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu pafupi ndi chipata cha Hamati.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 13:21
15 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere,


Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.


Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza.


Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere-Hatikoni ndiwo kumalire a Haurani.


Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?


Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.


popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m'chipululu cha Zini.


Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi).


kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi.


amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku chigwa cha Esikolo, nachizonda.


popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatule Ine pakati pa ana a Israele.


ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum'mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati;


Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.


Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mzindawo, nakhala m'mwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa