Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
Numeri 2:3 - Buku Lopatulika Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu. |
Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;
Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.
Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.
Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Nasoni mwana wa Aminadabu.