Numeri 3:38 - Buku Lopatulika38 Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201438 Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa38 Amene ankamanga zithando zao patsogolo pa chihema cha Mulungu kuvuma kotulukira dzuŵa, kutsogolo kwa chihema chamsonkhano, anali Mose ndi Aroni pamodzi ndi ana ake a Aroni. Iwoŵa adaŵapatsa udindo wosamala kayendetsedwe ka chipembedzo m'malo opatulika, zonse zimene ankayenera kuchita m'malo mwa Aisraele. Munthu wina aliyense wofika pafupi ankayenera kuphedwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero38 Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa. Onani mutuwo |