Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 2:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 2:3
19 Mawu Ofanana  

Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:


Ana a Leya ndi awa: Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.


Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.


ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe)


Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.


Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,


Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,


Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka.


Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.


Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa.


Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.


ndi ngʼombe zothena ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Naasoni mwana wa Aminadabu.


Aramu anabereka Aminadabu, Aminadabu anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni.


Aminadabu abambo a Naasoni, Naasoni anali abambo a Salimoni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa