Numeri 2:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.” Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Aisraele, pomanga zithando, aliyense azimanga pafupi ndi mbendera yake imene ili ndi zizindikiro za banja la kholo lake. Azimanga moyang'anana ndi chihema chamsonkhano, tsono mochizungulira. Onani mutuwo |
Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo.
Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino