Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Aisraele, pomanga zithando, aliyense azimanga pafupi ndi mbendera yake imene ili ndi zizindikiro za banja la kholo lake. Azimanga moyang'anana ndi chihema chamsonkhano, tsono mochizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 2:2
23 Mawu Ofanana  

Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu; aika mbendera zao zikhale zizindikiro.


Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika padziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,


Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira padziko lake.


koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.


Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.


Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi.


Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.


Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.


pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.


Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;


kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.


Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapite njirayi kufikira lero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa