Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:12 - Buku Lopatulika

12 Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda, ndiye adapereka zopereka zake pa tsiku loyamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.


Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.


Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lake, apereke zopereka zao za kupereka chiperekere guwa la nsembe.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;


ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni;


mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni,


ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa