Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Numeri 15:30 - Buku Lopatulika Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. |
Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.
Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.
Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.
Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho; chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.
Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.
Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.
Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.
Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.
Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.
Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.
Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.
Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.
Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.
Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.