Numeri 15:29 - Buku Lopatulika29 Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Mukhale ndi lamulo limodzi pa munthu aliyense amene alakwa mosadziŵa, pa mbadwa iliyonse pakati pa Aisraele ndi pa mlendo amene akhala pakati pao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo. Onani mutuwo |
Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji paphiri la Gerizimu, ndi ena pandunji paphiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.