Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 15:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Motero wansembe amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta munthu wolakwa mosadziŵayo. Akalakwa choncho mosadziŵa, amchitire mwambo wopepesera machimo, ndipo adzakhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:28
5 Mawu Ofanana  

natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.


nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.


Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa