Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 20:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Munthu akapita kwa wolankhula ndi mizimu yoipa ndi kwa wanyanga, nadziipitsa pakutsatira iwowo, ndidzamfulatira ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 20:6
17 Mawu Ofanana  

Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.


Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.


Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.


Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.


Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.


Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao.


pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.


Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;


Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa