Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 19:13 - Buku Lopatulika

13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa; iwo asandilamulire. Kotero ndidzakhala wosalakwa, wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 19:13
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.


Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.


Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.


Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.


Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye, ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa.


Chikopa changa chili ndi Mulungu, wopulumutsa oongoka mtima.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.


Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;


Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;


Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa