Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 19:12 - Buku Lopatulika

12 Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake? Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 19:12
19 Mawu Ofanana  

Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine; mundizindikiritse umo ndinalakwira.


Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.


Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.


Mphulupulu zinandipambana; koma mudzafafaniza zolakwa zathu.


Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.


Wonyoza mau adziononga yekha; koma woopa malangizo adzalandira mphotho.


Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.


Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!


Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa