Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:14 - Buku Lopatulika

14 Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma munthu akapha mnzake mwadala mwa njira yonyenga, aphedwe ndithu ngakhale wathaŵira ku guwa langa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma ngati munthu akonza chiwembu ndi kupha mnzake mwadala, ameneyo muchotseni ngakhale ku guwa langa lansembe ndipo aphedwe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:14
18 Mawu Ofanana  

Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.


Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.


Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.


Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje; asamuletse.


Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.


Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.


Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.


Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.


Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,


koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa