Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:13 - Buku Lopatulika

13 Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma ikakhala ngozi, kuti sadaganize konse zomupha mnzakeyo, angathe kuthaŵira ku malo amene ndidzakupatsani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma ngati sanachite dala, ndipo Mulungu analola kuti zichitike, iyeyo athawire ku malo kumene ndidzakupatsani.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:13
13 Mawu Ofanana  

Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?


Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.


Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.


Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa