Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 3:14 - Buku Lopatulika

14 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Nchifukwa chake ndikulumbira kuti mlandu wa banja la Eli sudzatha konse mpaka muyaya, ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:14
10 Mawu Ofanana  

Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.


Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa chihema changa ali pakati pao.


Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa