Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mlaliki 2:3 - Buku Lopatulika

Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.

Onani mutuwo



Mlaliki 2:3
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.


ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.


Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.


Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.


Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,


Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.