Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidaachita ntchito zazikulu. Ndidaamanga nyumba zambiri, ndi kudziwokera mipesa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:4
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.


Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.


Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.


Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,


ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;


Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.


Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mzinda wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.


Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.


Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi.


Tilawire kunka kuminda yamipesa; tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, makangaza ndi kutuwa maluwa ake; pompo ndidzakupatsa chikondi changa.


Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wampesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wampesa m'chitunda cha zipatso zambiri;


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa