Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yakobe adayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka zimenezi nzochepa ndiponso zamavuto, zosalingana ndi zaka za makolo anga pa nthaŵi yao yonse pamene anali moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:9
29 Mawu Ofanana  

ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.


Ndipo masiku a Isaki anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.


Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati?


masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.


Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi mu Ejipito.


Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.


Ine ndine mlendo padziko lapansi; musandibisire malamulo anu.


Malemba anu anakhala nyimbo zanga m'nyumba ya ulendo wanga.


Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.


Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.


Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.


Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.


Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.


Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m'thupi, sitili kwa Ambuye.


Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachite mdima, ndi mphamvu yake siidaleke.


Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.


Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa