1 Samueli 25:36 - Buku Lopatulika36 Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201436 Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutacha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa36 Abigaile adabwerera kwa Nabala nampeza m'nyumba mwake akuchita phwando lalikulu ngati la mfumu. Nabala anali wosangalala mumtima mwakwe, poti anali ataledzera kwambiri. Tsono mkazi wakeyo sadamuuze kanthu kalikonse mpaka m'maŵa kutacha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero36 Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha. Onani mutuwo |