Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:25 - Buku Lopatulika

25 Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Motero ndidaikapo mtima kwambiri kuti ndidziŵe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi m'mene zinthu zimakhalira. Ndidafunanso kumvetsa kuipa kwake kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa msala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa misala.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:25
17 Mawu Ofanana  

Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.


Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku.


Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwake kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.


Monga galu abweranso kumasanzi ake, momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake.


Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.


Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.


Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.


Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.


Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;


Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sungathe kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa