Mlaliki 5:18 - Buku Lopatulika18 Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Tsono chimene ndimachiwona kuti nchabwino ndi choyenera ndi ichi: kumadya, kumamwa, ndi kumakondwerera ntchito zonse zolemetsa zimene munthu umagwira pansi pano, pa masiku oŵerengeka a moyo wako amene Mulungu wakupatsa. Nchokhachi chimene ungati nchako, choyenera kulandira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake. Onani mutuwo |