Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 2:23 - Buku Lopatulika

nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

nadza nakhazikika m'mudzi dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kumeneko adakakhala ku mudzi wina dzina lake Nazarete, kuti zipherezere zimene aneneri adaanena kuti, “Adzatchedwa Mnazarete.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndipo anakakhazikika mu mzinda wa Nazareti. Pamenepo zinakwaniritsidwa zonenedwa ndi aneneri kuti, “Adzatchedwa Mnazareti.”

Onani mutuwo



Mateyu 2:23
20 Mawu Ofanana  

Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako;


Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.


Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.


Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.


Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete,


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.


Anayankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudasi yemwe, wompereka Iye, anaima nao pamodzi.


Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? Koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.


Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.


Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti.


nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.