Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumudzi kwao, ku Nazarete.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti.

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:39
11 Mawu Ofanana  

Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete,


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;


Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.


Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa