Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:19 - Buku Lopatulika

19 Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pilato adalemba chidziŵitso nachiika pamtandapo. Adaalembapo kuti, “Yesu wa ku Nazarete, Mfumu ya Ayuda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:19
14 Mawu Ofanana  

nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.


Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.


Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!


Pamenepo ansembe aakulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndili mfumu ya Ayuda.


nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu.


Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.


Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa