1 Samueli 1:11 - Buku Lopatulika11 nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Adalumbira kuti, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, muyang'ane kuzunzika kwanga ndipo muyankhe pemphero langa, osandiiŵala ine mdzakazi wanu. Ndithu mukandipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzampereka mwanayo kwa Inu Chauta masiku onse a moyo wake, ndipo pamutu pake sipadzapita lumo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.” Onani mutuwo |