Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 1:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti,

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 1:22
22 Mawu Ofanana  

Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,


wakusungira mtumiki wanu Davide atate wanga chimene mudamlonjezacho; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.


Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti,


ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.


nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa.


kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.


Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataye mmodzi.


Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.


umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m'malembo oyera,


Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa