Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
Mateyu 10:3 - Buku Lopatulika Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; |
Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.
Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;
Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho.
Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.
Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma.
Ndipo zitatha izi Iye anatuluka, naona munthu wamsonkho, dzina lake Levi, alikukhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.
Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.
Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?
Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?
Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.
Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.
Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.
ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;
Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: