Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 1:48 - Buku Lopatulika

48 Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Natanieli anafunsa kuti, “Kodi mwandidziwa bwanji?” Yesu anayankha kuti, “Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 1:48
14 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;


Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.


Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mzinda wa Andrea ndi Petro.


Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.


Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira.


ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.


Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?


Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.


zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa