Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 1:47 - Buku Lopatulika

47 Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Pamene Yesu adaona Natanaele akubwera potero, adati, “Mwamuwonatu Mwisraele weniweni wopanda chinyengo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Yesu atamuona Natanieli akuyandikira, anati kwa iye, “Uyu ndi Mwisraeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 1:47
13 Mawu Ofanana  

Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.


Indedi Mulungu achitira Israele zabwino, iwo a mtima wa mbee.


ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.


Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.


Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu;


Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.


ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;


Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwe bodza; ali opanda chilema.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa