Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 18:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 18:17
27 Mawu Ofanana  

Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,


ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayende m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.


Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;


Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwao.


Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye.


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Ndinalembera inu m'kalata ija, kuti musayanjane ndi achigololo;


Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?


Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.


makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa