Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:17 - Buku Lopatulika

17 Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:17
28 Mawu Ofanana  

ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.


Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.


Koma m'mene iye anatulukamo, sanathe kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya mu Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.


Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.


Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.


Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.


Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.


Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Koma Petro anakhala chigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.


Koma kutacha, panali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti.


Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine:


Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.


Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Aleksandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.


Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.


pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse;


Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.


Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.


ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa