Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:56 - Buku Lopatulika

56 mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

56 mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

56 Pakati pao panali Maria wa ku Magadala, Maria mai wa Yakobe ndi Yosefe, ndiponso mai wa ana a Zebedeo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

56 Pakati pawo panali Mariya wa ku Magadala, Mariya amayi ake Yakobo ndi Yosefe ndi amayi a ana a Zebedayo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:56
13 Mawu Ofanana  

Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?


Ndipo Maria wa Magadala anali pamenepo, ndi Maria winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawo.


Ndipo popita tsiku la Sabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda.


Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.


Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.


Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.


ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,


Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.


Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa