Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 21:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 M'maŵa mwake Paulo adatitenga kupita kwa Yakobe. Akuluampingo onse anali kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 21:18
12 Mawu Ofanana  

Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;


ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.


Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.


Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine:


Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.


Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:


Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.


Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.


popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;


Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.


ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa