Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Masalimo 83:3 - Buku Lopatulika Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuchitira anthu anu upo wonyenga. Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda. |
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.
Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeke wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo;