Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 1:10 - Buku Lopatulika

10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tiyeni tiwachenjerere. Tikapanda kutero adzachuluka kuposa ife, ndipo ngati kutakhala nkhondo, adzadziphatika kwa adani athu nadzamenyana nafe, kenaka nʼkudzachoka mʼdziko muno.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:10
13 Mawu Ofanana  

Akola eni nzeru m'kuchenjera kwao, ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.


Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.


Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.


Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa;


Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.


Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;


Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.


Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa