Eksodo 1:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Tiyeni tiwachenjerere. Tikapanda kutero adzachuluka kuposa ife, ndipo ngati kutakhala nkhondo, adzadziphatika kwa adani athu nadzamenyana nafe, kenaka nʼkudzachoka mʼdziko muno.” Onani mutuwoBuku Lopatulika10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.” Onani mutuwo |
Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa?