Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 1:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iyo inati kwa anthu ake, “Taonani, Aisraeli achuluka ndipo ndi amphamvu kwambiri kuposa ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mfumuyo idauza anthu ake kuti, “Aisraeleŵa akuchuluka kwambiri, ndipo ndi amphamvu kupambana ife.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:9
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abimeleki anati kwa Isake, “Muchoke pakati pathu chifukwa mwasanduka wamphamvu kuposa ife.”


Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu.


Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa.


Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.”


Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu, koma popanda anthu kalonga amawonongeka.


Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.


Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.


Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake.


Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa