Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 1:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pambuyo pake padaloŵa mfumu ina imene sidadziŵe za Yosefe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:8
10 Mawu Ofanana  

amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.


“Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani.


Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.


Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraeli, ndipo ndaona mmene Aigupto akuwazunzira.


Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo.


Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto.


Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.


Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga.


Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa