Eksodo 1:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya. Onani mutuwoBuku Lopatulika11 Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao. Onani mutuwo |