Masalimo 69:18 - Buku Lopatulika Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola; ndipulumutseni chifukwa cha adani anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola; ndipulumutseni chifukwa cha adani anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Senderani pafupi, mundiwombole, mundipulumutse kwa adani anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bwerani pafupi ndi kundilanditsa; ndiwomboleni chifukwa cha adani anga. |
Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?