Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:1 - Buku Lopatulika

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya? Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe? Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:1
23 Mawu Ofanana  

Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga; ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.


Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?


Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.


Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi, pakuti palibe mthandizi.


Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.


Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.


ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa.


ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.


Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.


Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.


Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?


Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa