Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 14:8 - Buku Lopatulika

8 Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Inu Chauta, amene muli chikhulupiriro cha Aisraele, ndiponso Mpulumutsi wao pa nthaŵi ya mavuto, mukukhaliranji ngati mlendo m'dziko lino, ngati wapaulendo wogona usiku umodzi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso, chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno? Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 14:8
25 Mawu Ofanana  

Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?


Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.


Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;


Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.


Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.


Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.


Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.


Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israele, Mpulumutsi.


Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.


Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.


Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.


Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu.


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:


Pamene anakweza maso ake anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mzinda; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? Ufumira kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa