Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:12 - Buku Lopatulika

12 Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga; mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga; mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nkhunzi zambiri zandizungulira. Adani amphamvu ngati nkhunzi za ku Basani andizinga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira; ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:12
14 Mawu Ofanana  

Yehova, mudazipenya; musakhale chete, Ambuye, musakhale kutali ndi ine.


Fulumirani kundithandiza, Ambuye, chipulumutso changa.


Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.


Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.


Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola; ndipulumutseni chifukwa cha adani anga.


Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi; ngati m'manja anga muli chosalungama;


Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga. Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa.


Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.


Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;


Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani.


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa